DSeven Smith

DSeven Smith

Share

•Woyimba
•Mphunzitsi wazachilengedwe

23/05/2026

MTSIKANA WINA PA DEPORT(Lena & Daniel)
Part 2

Kwa zaka ziwiri, chilichonse chinkaoneka ngati changwiro.

Koma chikondi chimasintha moyo ukakhala wovuta.

Daniel adapeza ntchito yovuta atamaliza koleji. Ankagwira ntchito usiku kwambiri, amakhalira kuyankha mafoni osatha, ndipo pang'onopang'ono anayamba kukhala kutali ndi Lena osazindikira. Lena anayesa kumvetsetsa, koma anayamba kumva kuti muchikondimo alimo yekha ingakhale atakhala pambali pa Daniel.

“Simukumachedza nane,nso masiku ano🙁” adatero usiku wina Lena

“Ndimakhala otopa ine,” anayankha Daniel.

Koma kutopa, kunatsanduka kutsachedza(kusayankhulana) pang'onopang'ono.

Kenako kunabwera Marcus, mnzake wa Lena wakuntchito. Anamvetsera nkhani zake, anayetsetsa kumupanga kuti atsekeko, koma anaona chisoni chomwe Lena ankayesa kubisa.

Daniel anaona kusintha nthawi yomweyo.

“Kodi wayamba kumukonda?” anafunsa mokwiya madzulo ena.

Lena anaoneka wokhumudwa.😔 “Ndimafuna kuti mundimvetse momwe amachitira.”

Mawuwo anamukhudza Daniel kwambiri kuposa momwe ankayembekezera.

Kwa nthawi yoyamba, anazindikira kuti chikondi sichinali chongofuna kukhala limodzi koma chimakhudzanso chidwi, kuona mtima, ndi khama.

Koma m'malo mokonza zinthu mofatsa, anakangana kwambiri.

Pomaliza pake, Lena ananong'oneza mawu omwe anakhuza Daniel kwambiri.

“Mwina tingosiyana"💔🤦

Ndipo motero, mtsikana yemwe anakumana naye pa siteshoni ya basi yamvula anatuluka m'moyo wake.🚶🤧

Dikirani part 3...
Osaiwala kupanga:
A. LIKE kuti mutipatse chilimbikitso chobweretsa part inayo
B.FOLLOW kuti zisamakuphonyeni
C.SHARE kuti anzanu anzanu awone nawo nkhani zabwinozi

Want your public figure to be the top-listed Public Figure in Lilongwe?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Category

Telephone

Address

Lilongwe