STORY TIME
Humble cee the stories writer
Official page
Let's change the world
Follow the page
musicfylite.com for more
14/05/2026
#πΉ *THE WRONG SACRIFICE*βΌοΈπΉ
Chapter 05
Story Done by
LND CHIKUNβοΈFt STEPHANIE
0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
ππππππππππππππππππππππ
_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯........
π₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύ
Galimoto lidafika pamsi pa nthaka pomwe pamaoneka ngati dziko lina ndipo kunja kumaoneka ngati masana , pamene madalitso ndi mkulu uja amanyamuka kunyumba m'dima utayamba .
Maditso ndimkulu unja adatsika galimoto lija ndipo madalitso amadzimva ngati wafika ku America, amati adayang'ana chakutali amaona miseu yolowana lowana ndi ma building opakidwa utoto wokongola komanso yosanjikana.
Apa mkuti akungotsika kumene galimoyo. Mkulu uja adali otanganidwa ndi zochitika mugalimoto muja ndi adachedwa kutuluka , apa mkuti madalitso akudzimva ngati ndibwana kuti wa lemera kale malingana ndi komwe adali , . Amaona anthu ena owoneka mwachizungu , ena amaoneka mwachikaladi. Aliyense amaoneka osamba mwamakobidi , atawerama kudziyang'ana adayamba kudzichitira manyazi ekha .
Kutsogolo kwa galimoto kudali building yayikulu koma yomangidwa mwamakono , pomwe padayima galimoto padali magalimoto ochuluka omwe adapangidwa Park, koma padalibe galimoto ngati lomwe limapezeka kudziko komwe tachoka ngati passo , vits, ndi achina starlet,. Ayi magalimoto omwe amapezeka ndi ngati ma Toyota fortune, v8, range lover , rexus. Ndi mitundu yina yoti pa msika ikuyambira 120million .
Pena matha amandigwira maka ndikayang'ana magalimoto onsewo koma pa bwalopo padalibe nkhope ya munthu aliyense , ndimazifunsa kuti kodi Eni magalimoto ali kutiko .
Ndili muphokoso la mafunso ndidangomva kulira kwachitseko cha galimoto yomwe ndidakwera modzidzimutsa .
Ndidatembekira kuseri komwe mkulu uja amayenera kutsikira . Ndidamuwona wayenda kudzafika pomwe ndidayima mozungulira galimoto , koma akupumira m'mwamba ngati watopa .
Phwanga eko vala ichi , adandipatsa China chake ngati chimalaya cha ma batani mikoyayitali , ndidavala mophatikiza zovala zanga mkati.
Nawonso adali atavala kale , mkutheka ndi zomwe zimawachedwetsa kutsika mugalimoto muja mwachangu .
Nditavara adandiyang'ana mkundisekelera kenako adandilozera khomo lachinyumba chokongola chija .
Tonse tidayambira limodzi kuyenda , nditangolowa ndidawona ndendende ndizomwe ndidaona kumaloto zija .
Ndidaona anthu ambiri omwe adavara zovala ngati zomwe tidavara , ndidapatsidwa ndendende malo ngati akumaloto omwe ndidapatsidwa . Aliyense yemwe adandiyang'ana amandiona ndithu ngati mlendo basi . Chodabwitsa chidali choti mudali anthu ambiri koma mudalibemo phokoso mudali ziiiiiii.
Kutsogolo kwa gome kudali chi mpando chokongola kwambiri, koma padali munthu onenepa kwambiri , mkulu ndidalowa naye uja adadzipezera malo , koma ineyo adandikodola mkulu adali kutsogolo uja , ndidayenda mukanjira komwe kadali pakati pa anthu omwe adakhala mogawanikana , ndidafikira kutsogola mkuyima pomwe pafupi ndipomwe padakhala mkulu uja .zikuoneka kuti munthu yemwe adali kutsogolo uja zolinga zanga adali akuzidzi chifukwa adayankhula mau otere..
Ngati ukufuna kulemera ukuenera kukhetsa mwazi umenewo ndio mwambo wakuno koma ngati sutelo udzakhara kapolo wadziko ndipo dziko lidzakuonelera ukuvutika kotelo ndikukupatsa chinthu ichi kuti chikakupase chuma chochuluka uko kudziko udzakhara. m'modzi mwa anthu olemeletsetsa kudziko
Ndikuyenela kukudalitsa ndi madzi awa ndikukupatsa mphamvu zochuluka zomwe zidzathe kutetezera chuma chako. ndikukupasa izi kamba kakuti tsopano ndiwe mwana wanga koma chinthu China ukuenera kupeleka msembe ndipo msembe imeneyo Tifuna chala chako chaching'ono chimodzi cha phazi lakumanja koma choyamba landira madzi odalitsidwa. Ine monga mfumu yakumidima ndikukuthira madzi awa pamutu wako monga mdalitso wanga.
Anali madzi otentha kwambili omwe atangondithira pamutu panga ndinayamba kulira nawo......
Ndidalira mosisima misonzi yidayamba kutsika , mantha adandigwira . Ndiluze chala zoona chifukwa cha chuma, ndidadziyankhulira .
Kuopa kukhala kapolo ndidalandira chinthu chija koma chimaoneka ngati mphika madali madzi ofiira .
Adayitana nzakazi wake mmodzi yemwe adamuyimira kumanzere kuti adzachotse chala , . Ndidanthunthumira ndi mantha . Koma ndikamva za chuma ndimalimba mtima . Mzakazi uja adabwera kudzadula chala changa ndi chimpeni .
Atangondidura ndidagwa pamsi kulira , m'malo modzandigwira kundimvera chisoni. Ndipomwe anthu onse adali mkati muja amasangalala kumaomba mmanja , eshiiiii koma ufiti winawu , ndidakumbukira agogo anga anazunga , kuti akadakhala alipo bwenzi akundithandiza kulira .
Adatenga chala chija mkuchiponya muka mphika kena . Nthawi yomweyo adatenga magazi omwe amawatchezekera achala changa mutambula , mkundimwetsa , ndidazimva ngati chilombo China chake chopanda chisoni .
Ndidapatsidwa malangizo kwa mfumu ija . Udzalemera kwa zaka five kwinako udzafa poti wadzipereka wekha moyo wako .
Zidandinyansa poti ndidali nditavomera kale , koma mwayi okana adandipatsa kumayambiliro ndisadayambe zonse .
Kenako adandipatsa pokhala , ndipo mfumu ija ikamayankhula imayankhula chiyankhulo chosamveka koma chodabwitsa ineyo ndimamva nawo .
Amayankhula ngati akutidalitsa ngati momwe amapangira akatolika muja tonse timayankhira limodzi ndithu , .
Pomwe ndidakhalapo tidalipo anthu anayi omwe timaoneka kuti tikuyamba kumene koma anzanga ndidawapeza atawadalitsa kale chifukwa ndidaona aliyense kutsogolo kwake kuli ka mphika .
Tidagwada kukhala ngati tikuyipembedza mfumu yomwe idali kutsogolo ija tonse , koma ineyo ndidali mu ululu osaneneka chala chija chimandipweteka koma padalibe magazi aliwonse sindikudziwa kuti adandipanga chani , ndimaoneka olumala chala chimodzi ndidalibe .
Tidamaliza kupembedza tonse tidayamba kutuluka , ndimaona anthu akunditchingira kutsogolo ndi moni , amvekere your welcome akundimwetulira , azungu makaladi akazi wokongola eshi kumandi sekelera .
Tidayenda mobalalikana koma molunjika khomo lotulukira .
Ndimaoneka kuti aliyense akundikonda , tonse oyamba kumene timalandira ma welcome .
Tidatuluka panja pomwe padali magalimoto amtengo wautali , aliyense amalunjika komwe kudayimikidwa galimoto lake , ine ndidatsatira msana wamkulu yemwe ndidabwera naye .
Tidakwera galimoto lathu lomwe tidabwera nawo , panja padali ziii aliyense atakwera mugalimoto lake , . Kenako magalimoto aja amakhala ngati akukankhidwa ndi mpweya kumakhala ngati akuwuruka . Ine mantha ndidalibe mtima wanga ndimaumva kulimba mtima ndimazimva kuti nditha kupha munthu koma osagwedezeka . Kenako yathu yokha yidapezeka pomwe tidafikira pamayambiliro padali pakati pa msewu ndithu tala koma kudalibe galimoto lililonse. Tidatembenuka ngakhale magalimoto omwe tidanyamukira nawo limodzi ku kachisi kuja sidawaonenso pomwe tidafikirapo .
Tidatembenuka ulendo waku nyumba ka mphika kanga nditakayika mpheche peche mwanga ....
Titafika kunyumba mkulu uja adandiuza kuti chovala chomwe ndidavara chija ndichitenge ndidzikavala ndikamapita kopembedza . Ndidadziyang'ananso kuphanzi ndidaonadi kuti ndilibe chala ndendende zakumaloto ..........
Next part 6...
Let's share to all groups
#πΉ *THE WRONG SACRIFICE*βΌοΈπΉ
Chapter 03
Story Done by
LND CHIKUNβοΈFt STEPHANIE
0998242764/0999739805 *Home of Super stories Gp* INCLUDING *ADMIN PANEL STORY GROUP*
ππππππππππππππππππππππ
_MORE COMMENT MORE SHARE MORE_π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯π₯........
π₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύπ₯Ύ
Juliana dekha dekha pita ukakoleze moto ndi tapiwa ?,,,,,,,,oooh chabwino.
Kenako a neighbour adabwelera kunyumba ya siwa komwe adapeza anthu adzadzana chifukwa cha mfuwu wa agogo a juliana . Ma neighbour atatu achimuna adawakokera kuseri agogo ajuliana kuti amve programme.
Mayi akuntchito akudziwa?,,,,,,ayi ndithu sindinafikitse uthenga uliwonse ndikudalira inuyo anthu achimuna kuti mundithandizire, ok guys ma mammawa tipite kuntchito kwawo tikawafotokozere ,. Nanga mwambo wamaliro ukachitikira kutiko ?,,,,,,,,, kwathu kwa yasini ,,,,,,,,kodi akazi awo aja ndi akomweko ?,,,,,,,,,eya koma manda ndi osiyana ,,,,,,,, ok nde maliro alikutiko ?????? ,,,,,,ndawasiya ku mortuary ku Queens,,,,,,,,, ok ma phone awo adapezeka pa malo angoziyo?,,,,,,,,imodzi ya bambo ndilinayo ngakhale idasweka koma sim card ilipo,,,,,,,, tabweretsani simcard mwina tilumikizane ndi akuntchito kwawo .
Mzibambo mmodzi adatenga simcard ija mkuyika mu phone mwake , adayamba kuwona ma contacts , adapeza number yolemba kuti office ina idali yolemba kuti abwana. Ok tiyese yaku office ikakanika tiyese iyi ya abwanayi.
Kutruuuu...kutruuu....kutruuu...kutruuu . Hello this is agriculture office line muli bwanji Mr Adam ,,,,,,,,,,tili bwino koma ineyo ndine neighbour wa Mr Adam,,,,,,,,,,,,,can I help you?,,,,,,,, yes sir timafuna tikudziwitseni kuti Mr Adam achita ngozi ndipo amwalira pomwepo ndi akazi awo omwe moti tikunena pano matupi awo akusungidwa ku nyumba yachisoni ku Queens,,,,,,,,, ooooh which Mr Adam?..... what is happening ,,,,,,,,,,,, eshiiii sorry sir adali ndi ulendo opita kumudzi ,,,,,,,,,yes offcoze zaulendo wawo ngakhale ku office kuno tikudziwa ,,,,,,,,,,, achita ngozi pa round about ya gingery pa fupi ndi factory ya pa universal busicults ,,,,,,,,, eshiiiiiii ok nde madongosolo ndi otani anamfedwa ,,,,,,,,, timafuna thandizo la nyumba ngati bokosi komanso kutinyamulira zovutazi kukatisiyira kumudzi ,,,,,,,,,,, ok pompano tikutumiza galimoto litenge matupi onse likasiye kunthunzi funeral .
Atadula foni , adalongosolera anzawo za dongosolo lakuntchito , ndipo adapita kukakhala pamsi kudikilira akuntchito .
*kumudzi kwa yasini?*........
Agogo amadalitso adayimbira foni alongo awo kuwadziwitsa za imfa ya mwana wawo ndipo alongo awo adaupereka uthenga kwa achibare komanso amfumu , zinthu zidachitika mwachangu powopa kumusokoneza madalitso adamuuza kuti apite akakhale kunyumba kwa alongo awo a gogo ake , .
Madalitso poganizira mizimbe yomwe idali kudimba kwa alongo awo agogo ake adapita mwa msanga .
*Chirimba*...
Galimoto lokulirapo lidafika lol lolembedwa kuti agriculture komanso kujambulidwa mbewu zosiyana siyana pa chitseko chake .
Adanyamula anthu kuphatikizapo agogo amadalitso ngati namfedwa. Komanso akuntchito a department yawo ena adali momwemo.
Galimoto lidanyamuka , adanyamula matupi awo kupita kukasiya kunthunzi kuti akakonze bwino bwino . Kenako adabwerera , atangofika kunyumba adapeza ampingo aziyambitsa kuswa ma kolasi .
Nyimbo zija zimamveka ndithu kunyba ya aneighbour komwe kudagona juliana. Juliana sadagone kumvetsera nyimbo zija zomwe zimayimbidwa mwa nthetemya koma zina mwanyimbozo mumatchulidwa maliro maliro choncho , zomwe zidayamba kupereka maganizo ofoora thupi lake juliana.
Ma m'mawa kutacha neighbour adathamangira kunyumba kukakonzekeretsa juliana kuti akapite naye akamakanyamuka kukatenga maliro .
Atafika adamuyitanira ku bafa juliana, atamaliza kumusambitsa , adamuveka zovala zomwe adapatsidwa ndi agogo ake , atamaliza kumukonzekeretsa , adadya chakudya limodzi ndi anzake . Tapiwa amamuuza juliana kuti pepa , chifukwa choti amamva kulira kunyumba kwa juliana , izi amakamba pokumwa tea . Atamaliza mayi atapiwa adamutengera juliana kunyumba ya siwa komwe adakapeza kuli anthu ochuluka koma nkhope za makolo ake sadazione .
Agogo ake amamveka ku sasa mau ndi kulira , nthawi m'mene imati 9:00am galimoto lalikulu tidatulukira pa khomo la Adam. Ndipo mkati mwa galimotomo mudayikidwa ma bokosi awiri . Anthu achuluka pamodzi ndi ampingo adakwera . Anthu omwe adatsalira adasamala katundu yemwe adamutulutsa uja mnyumba .
Galimoto lidaponda nthaka lapa nthunzi funeral. Onse adatsika ndipo ma bokosi awiri aja adatsitsidwa .
Adalowetsa munyumba yachisoni ma bokosi aja. Ampingo sadasiye kuyimba atakhala malo odikilira , agogo amadalitso adalowa mkati kuti akatsimikize kuti matupi omwe akuyikidwa bokosi ndi awodi ndithu.
Kenako adatuluka koma atagwiridwa uku ndi uku kwinaku akulira kwambiri, milandu idali yosayamba polirapo , mwandirakwira kuphera mwana wanga ondithandiza ine . Mukudziwa inu mzimayi police amakhala ndi nthano zake .
Madotolo adapempha anthu onse kuti abwere adzaone nkhope ndipo aliyense yemwe adalowa mkutuluka opanda misonzi sadapezekepo , zidalibe kuti ndi wamamuna , nkhalamba , namwali ,kapena wokalamba .
Anthu adalira momvetsa chisoni , kuona nkhope ya Mr Adam ikuwoneka bwino bwino ngati angogona ndithu .
Kenako adatulutsa mabokosi onse mkuwakweza galimoto lalikulu , anthu onse akuntchito adakwera coastar , pamene ena onse adakwera chi trak chija . Agogo amadalitso adakhala kutsogolo atafundira msalu . Naye juliana adakhala ndi agogo ake kutsogolo .
Galimoto lidanyamuka kutenga msewu wa mulimbe , nyali zikuyaka mwa chidziwitso cha danger . Ampingo amayimba ndithu ulendo kuperekeza wokondedwa awo . Atafika mu limbe adakhotera msewu wa zomba uyo kwakachere uyu msewu wa chiradzulo boma mpaka adakafika mwa yasini , koma atakhotera msewu opita kwawo msewu onse amapeza anthu atayimilira ngati akudikira president, nkhope zawo zili za chisoni magalimoto adachepetsa liwiro , ndipo anthu adapeza mpata omatsatira kwinaku akulira , azimayi atafundira kumutu msalu akulira . Atafika pakhomo , asadatsitse adadya khonde ndi akuchika agogo a madalitso .
Tipepese zatigwera maliro afika ndithu , anthuwa manda ndi osiyana mwaganiza motani mmbuyo muno ,,,,,,,,,,,, timaganiza kuti mayiwa titenge tikalilire kwathu ,,,,,,,,,,ok ndekuti wathuyi timutsitsira pano inu mudzipitilira ndi wanuyi ,,,,,,,,, oooh chabwino . Onse adabalarika kukamufotokozera oyendetsa madongosolo .
Pepani akuntchito komanso ampingo , akuchikazi apempha kuti waoyi akalilira kwawo . Anthu onse adadzuma amvekere ,. Kufuna kupereka chintchito chachikulu kwa akumpingo ndi akuntchito kumeneko , . Ngakhale zidali choncho chiganizo sichidasinthe.
Adapempha achinyamata kutsitsa thupi la Mr Adam kulowetsa mnyumba , kenako ena adakwera galimoto lija kuperekeza thupi la mayi Adam kwawo midzi idali yoyandikana .
Kumenekonso adapanga siwa yawo , akuntchito adapereka chilichonse chofunikira masiwa onse .
Juliana adadziwa tsopano chomwe chidachitika mumsewu akupita ndi maliro kumudzi naye adalira mokweza , . Midzi iwiri idali pachisoni ndi imfa yoopsa ngati imeneyi .
Maliro adapempha ampingo kuti ayike masiku osiyana kuti akhale ndi mpata oyendetsa mwambo wawo , koma achipatala adakana kuti sipakufunika kuchedwa chifukwa angozi sagonekedwa m'nyumba .
Ampingo adagawana komanso akuntchito adagawana . Chirichonse chidayenda ndi mwambo oyenera , padalibe chovuta .
Nthawi mmene imakwana 16:00pm mkuti atayika maliro akuntchito , adabwera pasiwa kudzadya chakudya chomwe chidakhonzedwa mochedwa . Nkhata adayika madalitso ndi juliana adalilitsa anthu atalira momvetsa chisoni .
Anthu atamaliza mwambo akutauni onse adakwera ma galimoto akuntchito kwa Mr Adam ndipo akuntchito pochoka adasiya mawu kwa agogo kuti , madangosolo akuntchito abwere pakatha week imodzi adzalongosole .
Madalitso ndi juliana adatsala kumudzi ndi agogo moyo udayamba kusokonekera .
Umasiye udayambika , akubanja akuchikazi adapempha kuti akatenge ana kutengera miyambo yawo koma juliana ndi madalitso adakana ponena kuti iwo adazolowera kukhala ndi agogo awo akuchimuna . Izi zimachitika chifukwa nawonso mayi awo amakonda kusamala kwambiri kuchimuna .
Week idatha agogo akuchimuna ndi akuchikazi adatengana kupita kuntchito komanso kupolice kukayendetsa program yokhudza ndalama za insurance. Kenako adapita kuntchito kukalongosola ndalama zakuntchito .
Konseku adakonza koma adauzidwa masiku akatenga ndalama.
Madalitso adaphunzira khasu ndipo juliana adamutengera transfer kukamusiya ku sukulu ya boma . Moyo okumwa tea udasintha . Pena amapita ku sukulu osadya .........
Next part 4.....
Let's share to all groups
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Contact the public figure
Telephone
Website
Address
Ntaja