RedArc Media Blog
Redarc Media Blog is an independent Social Media News Agency based in Malawi.This is Your one-stop destination for the Breaking News and funniest insights.
25/07/2026
MAGANIZO ANU NDI OTANI?
Lero pa 25 July 2026 Nyasa Big Bullets yagonja pa Dedza Dynamos 1-0 ndi Goshen,kuoangitsa kuti ulendo wa usapheka uja uthele pomwepo.
Pakadali pano Bullets inapeza international Coach yemwe pomukonda amati Wada wada.
Tinene kuti kaseweledwe ka Bullets kaa ndi Coach Plan kuti akusakasaka moyichunila timuyi? kapena kuti Coachyu zikumuvuta?
Ena akuti vuto ndi Osewera kuti Madolo anachoka, ndipo Timuyi ikufunika Osewela ena? inu mutipo bwanji?
(Tikufuna Owutsata okha,osati omangosapotela dzina,tikuzepulani)
25/07/2026
Masewero amu mpikisano wa FDH Bank Premiership omwe aseweredwa lero pa 25 July 2026 ayenda motere.
Pa Dedza Stadium,timu ya Goshen Dedza Dynamos yagonjetsa FCB Nyasa Big Bullets 1-0 ndi chigoli chokhacho chomwe chidagoletsedwa ndi Marco Chiwaya mu mphindi 41.
Nayo Blue Eagles yapambana itagonjetsa Red Lions ndi zigoli 3-2 pa bwalo la Nankhaka Stadium.Tonic Viyuyi ndiyemwe anagoletsela ma Eagles zigoli ziwiri mu phindi 50 ndi 88,pomwe Shamiuna Watch adabwela pa mphindi 61.
Ndipo Shukurani M***a ndi Matamandi Mwatchipitsa ndiwomwe anachinya chigoli chimodzichimodzi mbali ya Red Lions.
Chitipa United yapambana nayo pakhomo 1-0 kugonjetsa timu ya Ekhaya FC kuchigoli chomwe chinabwela mu mphindi 56 kuchokela kwa Chancy Kaonga.
Mu nthawi yopweteka kwambiri, nayo Civil Service United yagonja pakhomo ndi timu ya Moyale Barracks yomwe inachinya chigoli mu nthawi yowonjezela 90+1 kuzela kwa katswiri Black Alisen.
Emmanuel Makhamla ✍️
Unbeaten Fc,Coach of the Month FC 🤔
25/07/2026
CHIKANGA AGONA NDI ZIDZUKULU ZAKE ZITATU
Bwalo la milandu ku Lilongwe lagamula bambo Kupata Chikanga azaka 40 kuti akakhale kundende kwa zaka 21 chifukwa chopezeka olakwa kuti amagonana ndi atsikana achichepele azaka 14,10 komaso 14 mwezi wa May ndi June chaka Chino.
Bambo Chikanga amawanyengelela anawa powapatsa K500 maulendo onse omwe angakumane nawo.
Khotili lapeleka chigamulochi potengela kuti Bambo Chikanga ndi agogo awanawa.
Habib why koma😂
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Address
Blantyre
Chichiri