Shushe
Happy New year
26/01/2024
Banja la malemu a Kaphwiti Banda likuchita m'bindikiro ku Civil Registry ku Lilongwe kufuna kuti bwalo la milandu lifulumize nkhani ya malo awo omwe akulephera kutenga kwa Mama Cecilia Kadzamira.
Yemwe akuyimilira banjali, a Tapiwa Kaphwiti Banda watiuza kuti akuona ngati chilungamo sichikuyenda pa nkhaniyi yomwe anakayitula ku bwalo la milandu mu 2016 koma tsiku loyamba kumva mlanduwu silinakhazikitsidwebe kufikila lero.
Iwo ati ali ndi mapepala onse owonetsa umwini kuti malowa omwe ali ku Mchinji ndi awo ngakhale kuti a Kadzamira amati malowa anapatsidwa ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino a Hastings Kamuzu Banda ngati mphatso.
Banjali lati akukanika kulima pa malowa kamba koti panatengedwa chiletso kuwaletsa kugwirapo ntchito iliyonse ngakhale kuti ayesela kuchotsa chiletsochi katatu.
Banjali lati lipitilira kuchita m'bindikilowu mpaka mkulu oweruza milandu atamva madandaulo awowa ndikuchitapo kanthu.
(by Zuleika Nanguwo-Lilongwe: 01/26/2024)
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Contact the public figure
Telephone
Website
Address
Lilongwe