Kufunafuna chipulumutso

Kufunafuna chipulumutso

Share

CHIPULUMUTSO SICHOMPWEKA

25/08/2025

*WANZERU ATENGAPO KANTHU*
Company ina yomwe imachitisa mpikisano. Itaona K*t mzimayi wina wawina k10,000,000 idatumiza munthu wabambo woti akamukonzekeletse mayi uja zakalandilidwe ka ndalama ija poopa K*ti akamudzidzimutsa atha kumwalira kapena kukomoka ndichisangalaro!!!
Atafika bambo uja adalonjelana ndipo Macheza adayambika
*Bambo* ; Kod mayi munthu atakupatsani 1 million mungatani??

*Mayi* ; ndikhoza kusangalara kwambiri.
*Bambo* ; nanga 5 million??
*Mayi* ; eeeee ndikhoza kupita Ku China ndi banja langa kkkk
*Bambo* ; kkkkk ok nanga nditati ndakupatsani 10 million ??
*Mayi* ; mmmmmm nditha kupita kunja kumakatenga katundu nkumagulitsa.
Atacheza mwakanthawi bambo uja adawauza mayi aja kuti Mwawina 10 million kwacha.Ndipo mmayi adadumpha ndichimwemwe!! Pofuna kumuthokoza bambo uja mayi adati abambo inu ndinu abwino ndikupatsani 1 million pa ndalama yomwe ndawinayi!!
Bambo poyiganizila 1 million adagwa pansi nkukomoka poti kuncthito kwake amalandila 100 thousand ndipo ndikoyamba kuti apeze 1 million pakamozi!!!

# *PHUNZIRO* : bambo uyu amakonzekeretsa mayi kulandira 10 million pomwe iye asali okonzeka kulandila ndi 1 million yomwe!!! Chimodzimodzi masiku ano ambili Tili pa kalikiliki kukonzekeletsa amzathu za moyo wakumwamba pomwe Ife sitili okonzeka kuulandira!! Tikamamuuza mzathu K*ti lapa tidziyamba Kaye talapa ifeyo nkumauza bwino amzathu!!!
Khalani ndi tsiku lopambana ambuye akudalitseni nonse

*AMENπŸ‘πŸ‘πŸ‘πŸ‘*

25/01/2024

Kafukufuku waonetsa kuti anthu ambiri amene anabayitsa covid vaccine padziko lapansi akumakhala ndi vuto mu ubongo, mmisempha ngakhalenso spinal cord. Chodabwitsa; ambiri amene akupeza vuto limeneli ndi akazi.

Panopa boma la Malawi likusunga 1 million vaccine amene anapatsidwa ku America. Ndie munthu wagona ndi njala, amubayenso covid vaccine, angapulumuke?

Choyamba, tipemphe a boma athetse njala;
Chachiwiri, afufuze chimene chikuchitika kuti anthu ambiri amene abayitsa katemerayu azikhala ndi vuto la neurological disorder.

24/12/2023

*βœ“ MONI KUCHOKERA KWA AMBUYE MULUNGU* *WAMPHAMVUYONSE AMENE DZINA LAKE NDI YESU KHRISTU WAMOYO WA KU NAZARETI*

*βœ“ UTHENGA UWU SUKUIMILA MPINGO ULIWONSE* *KAPENA UTUMIKI ULIWONSE KOMA UKUPITA KWA OKHULUPILIRA* *ONSE .CHONDE TUMIZILANI OKHULUPILIRA ALIYENSE AMENE MUKUMUDZIWA*

*_MAPANGANO AMENE MULUNGU WAKHALA AKUPANGANA NDI ANTHU_*

*1. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI NOAH ( GENESIS 9:8-17)*

*βœ“ CHIZINDIKILO CHAKE UTA WA LEZA*

*2. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI ABRAHAMU*
*(GENESIS 17:9-14)*
*βœ“ CHIZINDIKIRO* *CHAKE MDULIDWE*

*3. PANGANO PAKATI PA MULUNGU NDI ISRAYELI* *( EZEKIEL* *20:12-13 )*

*βœ“ CHIZINDIKIRO* *CHAKE SABATA*

*4. CHIZINDIKIRO PAKATI PA MULUNGU NDI ANTHU AMITUNDU* *( AHEBRI 1:1-4)*

*βœ“ CHIZINDIKIRO CHAKE KUBWERA KWA MULUNGU YEKHA KUDZAKHALA MU* *DZIKO* *LAPANSI*

*βœ“ MZIMU WOYERA AKAKUTHANDIZANI KUMVETSETSA UTHENGA UWU ,NDIYE KUTI* *SIMUDZAPUTSITSIDWANSO NDI ZIPHUNZITSO ZONYENGA ZOMWE ZANGOTI* *BWEE PAKATI* *PATHU*

*FUNSO LILILONSE PA UTHENGAWU CHONDE FUNSANI KU +265 993 408834 .AMBUYE YESU KHRISTU AKUDALITSENI NONSE*

*SHALOM AND* *DIVINE GLORY!!!!!!*

*____________________________________________________________________________*

Want your place of worship to be the top-listed Place Of Worship in Machinga?
Click here to claim your Sponsored Listing.

Telephone

Website

Address


Machinga