Latest from Edmond Bitoni
POEMS FROM THE WORLD OF POETRY
NO SABOTAGE
100% ndikugwirizana nazo izi, nanenso zimandidabwisa ndithu kuti kodi sukuluyi anawa akuyiyendetsa bwanji???😣😣
Nanga makolo mukulekelera ana pa maphunziro, akalephera kumaloza chala aphunzitsi, ayi sizoona.
Mwana wina aliyense wa sukulu, kaa ukuziona kukula, ndiwe mwana wa sukulu basi mvera aphunzitsi ndipo uzichepese. Ngati sutelo kuchita bwino pa maphunziro kuvuta.
Iweyo ukupita ku sukulu ndiwe candidate chotengeranso Bluetooth ndi chani? Foni mkati, MANEB kuyesa mzako?
Lero waumbuza 40 points, ena kusenza mgolo kumene ndie chodandaula nd chani??? Chonsecho ukudziwa kuti umakhalira mma birthday, mowa, fodya mkati, Ndakwiya.
Ndikati ndikuuze mafoni analiko, koma sitnapange umu muchitiramu. Ndiwe candidate koma ukukhalira usana/usiku wonse Facebook, whatssap.
Malo moti waweluka zipita kunyumba ukadye, ukapedze nthawi yowerenga, ndipamene uliyaviyavi ndi m'nyamata/mtsikana zithandiza???
Ati Zibwenzi? Zibwenzi zake ziti zoyambira ku secondary kapena ku primary? Ati vis is Richard my beft friend. Owo Friend? Menemo sukudziwa kuti iye kwawo akafika amatani, ma results kubwera iye waoloka iwe wagweramo. Musinthe.
Kumakhala ma discussion. Inde kuthandizana zinthu anyamata ndi atsikana pokonzekera mayeso, lero ma discussion ake ndi afeki; mupeza ma hours ochuluka akukambirana nkhani zosagwirizana ndi sukulu.
M'mutumo m'malo moyikamo zolongosoka, za sukulu, basi busy zinthu zolaula, mayeso abwera empty brain.
Ineyo ndinauzidwa mawu kamodzi ndipo ndinagwira mawu. Zilinso kwa iwe kuwagwira kapena ayi:
MANKHWALA A MAYESO NDI KUWERENGA 🙌
APA NDI PAMENE TINGAZAZINDIKIRE KUTI KUUMBUZA 40 POINTS NDI CHAMUNA CHOMWE
Click here to claim your Sponsored Listing.
Category
Website
Address
Thyolo